Ciŵili, July 15
Weta ana a nkhosa anga.—Yoh. 21:16.
Mtumwi Petulo analimbikitsa akulu anzake kuti “Wetani gulu la nkhosa za Mulungu.” (1 Pet. 5:1-4) Ngati ndinu mkulu, tidziŵa kuti mumawakonda abale na alongo ndipo mufuna kuwasamalila. Komabe, nthawi zina mungamadzimve kuti simungakwanitse kusamalila udindo umenewu cifukwa cokhala wotopa kapena wotangwanika kwambili. Ngati zakhala conco, khutulilani Yehova nkhawa zanuzo. Petulo analemba kuti: “Ngati wina akutumikila, atumikile modalila mphamvu imene Mulungu amapeleka.” (1 Pet. 4:11) Abale komanso alongo anu angakumane na mavuto amene sangathetsedwe m’dongosolo lino la zinthu. Koma muzikumbukila kuti Yesu ‘mbusa wamkulu,’ angathe kuwathandiza kuposa wina aliyense. Angakwanitse kucita zimenezi palipano ndiponso m’dziko latsopano. Mulungu amafuna kuti akulu azionetsa cikondi kwa abale awo, kuwaweta komanso kuti akhale “zitsanzo kwa gulu la nkhosa.” w23.09 29-30 ¶13-14
Citatu, July 16
Yehova amadziŵa kuti maganizo a anthu anzelu ndi opanda pake.—1 Akor. 3:20.
Tizipewa kudalila nzelu za anthu. Tikamaona zinthu potengela maganizo a anthu, tinganyanyale Yehova na miyeso yake. (1 Akor 3:19) “Nzelu za m’dzikoli” nthawi zambili zimapangitsa anthu kusamvela Mulungu. Akhristu angapo a mu mzinda wa Pegamo komanso Tiyatira, anatengela kapenyedwe ka anthu owazungulila pa nkhani ya kulambila mafano, ndiponso zaciwelewele. Yesu anapeleka uphungu wamphamvu kwa Akhristu a m’mizindayi cifukwa colekelela zaciwelewele. (Chiv. 2:14, 20) Masiku anonso, timayesedwa kuti titengele maganizo oipa a dzikoli. Acibale athu na anansi athu, angamatinyengelele kuti tiphwanye malamulo a Yehova. Mwacitsanzo, angamatiuze kuti kutsatila zilakolako za thupi si nkhani yaikulu, komanso kuti malamulo a m’Baibo ni acikalekale. Nthawi zina, tingaganize kuti malangizo amene Yehova amatipatsa si okwanila. Tingafike pofuna ‘kupitilila zinthu zolembedwa.’—1 Akor. 4:6. w23.07 16 ¶10-11
Cinayi, July 17
Mnzako weniweni amakusonyeza cikondi nthawi zonse, ndipo ndi mʼbale amene anabadwa kuti akuthandize pakagwa mavuto.—Miy. 17:17.
Mariya mayi wa Yesu anali kufunikila mphamvu. Iye anali wosakwatiwa, koma anali kudzakhala na mimba. Cina, anali asanalelepo mwana, koma anali kudzalela mwana amene anali kudzakhala Mesiya. Ndipo popeza anali namwali, kodi akanafotokoza bwanji nkhaniyi kwa Yosefe amene anali kufuna kum’kwatila? (Luka 1:26-33) Kodi Mariya anapeza bwanji mphamvu? Anapempha thandizo kwa ena. Mwacitsanzo, iye anapempha mngelo Gabirieli kuti amuuze zowonjezeleka zokudza utumiki umenewo. (Luka 1:34) Posakhalitsa, Mariya anayenda ulendo wautali n’kupita “kudela lamapili” kudziko la Yuda kuti akaone wacibale wake Elizabeti. Elizabeti anayamikila Mariya, ndipo mouzilidwa na Yehova anakamba ulosi wolimbikitsa ponena za mwana amene anali kudzabadwayo. (Luka 1:39-45) Mariya anakamba kuti Yehova “wacita zamphamvu ndi dzanja lake.” (Luka 1:46-51) Yehova analimbikitsa Mariya kupitila mwa mngelo Gabirieli, komanso Elizabeti. w23.10 14-15 ¶10-12