LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
Tulukani
Loŵani
LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Takulandilani
Ici ni cida cofufuzila m'mabuku olembewa na Mboni za Yehova mu vitundu volekana-lekana.
Ngati mufuna kucita daunilodi, yendani pa jw.org.
  • Lelo

Citatu, July 16

Yehova amadziŵa kuti maganizo a anthu anzelu ndi opanda pake.​—1 Akor. 3:20.

Tizipewa kudalila nzelu za anthu. Tikamaona zinthu potengela maganizo a anthu, tinganyanyale Yehova na miyeso yake. (1 Akor 3:19) “Nzelu za m’dzikoli” nthawi zambili zimapangitsa anthu kusamvela Mulungu. Akhristu angapo a mu mzinda wa Pegamo komanso Tiyatira, anatengela kapenyedwe ka anthu owazungulila pa nkhani ya kulambila mafano, ndiponso zaciwelewele. Yesu anapeleka uphungu wamphamvu kwa Akhristu a m’mizindayi cifukwa colekelela zaciwelewele. (Chiv. 2:14, 20) Masiku anonso, timayesedwa kuti titengele maganizo oipa a dzikoli. Acibale athu na anansi athu, angamatinyengelele kuti tiphwanye malamulo a Yehova. Mwacitsanzo, angamatiuze kuti kutsatila zilakolako za thupi si nkhani yaikulu, komanso kuti malamulo a m’Baibo ni acikalekale. Nthawi zina, tingaganize kuti malangizo amene Yehova amatipatsa si okwanila. Tingafike pofuna ‘kupitilila zinthu zolembedwa.’​—1 Akor. 4:6. w23.07 16 ¶10-11

Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2025

Cinayi, July 17

Mnzako weniweni amakusonyeza cikondi nthawi zonse, ndipo ndi mʼbale amene anabadwa kuti akuthandize pakagwa mavuto.​—Miy. 17:17.

Mariya mayi wa Yesu anali kufunikila mphamvu. Iye anali wosakwatiwa, koma anali kudzakhala na mimba. Cina, anali asanalelepo mwana, koma anali kudzalela mwana amene anali kudzakhala Mesiya. Ndipo popeza anali namwali, kodi akanafotokoza bwanji nkhaniyi kwa Yosefe amene anali kufuna kum’kwatila? (Luka 1:26-33) Kodi Mariya anapeza bwanji mphamvu? Anapempha thandizo kwa ena. Mwacitsanzo, iye anapempha mngelo Gabirieli kuti amuuze zowonjezeleka zokudza utumiki umenewo. (Luka 1:34) Posakhalitsa, Mariya anayenda ulendo wautali n’kupita “kudela lamapili” kudziko la Yuda kuti akaone wacibale wake Elizabeti. Elizabeti anayamikila Mariya, ndipo mouzilidwa na Yehova anakamba ulosi wolimbikitsa ponena za mwana amene anali kudzabadwayo. (Luka 1:39-45) Mariya anakamba kuti Yehova “wacita zamphamvu ndi dzanja lake.” (Luka 1:46-51) Yehova analimbikitsa Mariya kupitila mwa mngelo Gabirieli, komanso Elizabeti. w23.10 14-15 ¶10-12

Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2025

Cisanu, July 18

Nʼkutipanga kukhala mafumu ndi ansembe kuti titumikile Mulungu wake ndi Atate wake.​—Chiv. 1:6.

Ophunzila a Khristu oŵelengeka anadzozedwa na mzimu woyela, ndipo amasangalala kukhala paubale wapadela na Yehova. A 144,000 amenewa azikatumikila pamodzi na Yesu kumwamba monga ansembe. (Chiv. 14:1) Malo Oyela m’cihema amaimila kudzozedwa kwawo monga ana a Mulungu pa dziko lapansi. (Aroma 8:15-17) Malo Oyela Koposa amaimila kumwamba kumene Yehova amakhala. “Nsalu yochinga” imene inalekanitsa Malo Oyela na Malo Oyela Koposa inali kuimila thupi la Yesu laumunthu limene linali kumulepheletsa kuloŵa kumwamba monga Mkulu Wansembe woposa onse wakacisi wauzimu. Pomwe Yesu anapeleka nsembe thupi lake laumunthu, anatsegulila Akhristu odzozedwa njila yopita kumwamba. Iwo ayenela kusiya matupi awo aumunthu kuti akalandile mphoto yawo kumwamba.​—Aheb. 10:19, 20; 1 Akor. 15:50. w23.10 28 ¶13

Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2025
Takulandilani
Ici ni cida cofufuzila m'mabuku olembewa na Mboni za Yehova mu vitundu volekana-lekana.
Ngati mufuna kucita daunilodi, yendani pa jw.org.
  • Cinyanja
  • Gawilani
  • Makonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenela Kutsatila
  • Mfundo Yosunga Cisinsi
  • Kusunga Cinsinsi
  • JW.ORG
  • Loŵani
Gawilani